Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali padziko lapansi.
2 Samueli 22:43 - Buku Lopatulika Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko, ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko, ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidaŵaperapera ngati fumbi, ndidaŵaphwanya ndi kuŵapondereza ngati matope amumseu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi; ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu. |
Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali padziko lapansi.
Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo.
Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala.
Mwachulukitsa mtundu, Yehova, mwachulukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.
Ndani anautsa wina wochokera kum'mawa, amene amuitana m'chilungamo, afike pa phazi lake? Iye apereka amitundu patsogolo pake, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga fumbi kulupanga lake, monga chiputu chouluzidwa ku uta wake.
Ndautsa wina wakuchokera kumpoto; ndipo iye wafika wakuchokera potuluka dzuwa, amene atchula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya.
Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golide, zinapereka pamodzi, ndipo zinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi.
Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.
Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzachita nkhondo, chifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzachitidwa manyazi.
Haya, haya, thawani kudziko la kumpoto ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova.
Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.
Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.