Zekariya 10 - Buku LopatulikaMalonjezo a kwa Israele 1 Pemphani kwa Yehova mvula, m'nyengo ya mvula ya masika, kwa Yehova wolenga mphezi; ndipo adzawapatsa mivumbi ya mvula, kwa yense zophukira kuthengo. 2 Pakuti aterafi anena zopanda pake, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto achabe, asangalatsa nazo zopanda pake; chifukwa chake ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa. 3 Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zake, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wake waulemerero kunkhondo. 4 Kwa iye kudzafuma mwala wa kungodya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi. 5 Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzachita nkhondo, chifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzachitidwa manyazi. 6 Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera. 7 Ndipo iwo a ku Efuremu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzachiona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova. 8 Ndidzawaimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzachuluka monga anachulukira kale. 9 Ndipo ndidzawafesa mwa mitundu ya anthu, ndipo adzandikumbukira m'maiko akutali; nadzakhala pamodzi ndi ana ao, nadzabwera. 10 Ndidzawatenganso kudziko la Ejipito, ndi kuwasonkhanitsa mu Asiriya; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Giliyadi ndi Lebanoni; koma sadzawafikira. 11 Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asiriya kudzagwetsedwa; ndi ndodo yachifumu ya Ejipito idzachoka. 12 Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m'dzina lake; ati Yehova. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi