Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 10:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asiriya kudzagwetsedwa; ndi ndodo yachifumu ya Ejipito idzachoka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asiriya kudzagwetsedwa; ndi ndodo yachifumu ya Ejipito idzachoka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pamene azidzaoloka nyanja ya ku Ejipito, ndidzathetsa mafunde a pa nyanjayo, madzi onse a mtsinje wa Nailo adzaphweratu. Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha, ndipo ndodo yaufumu ya Ejipito idzathyoka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Adzawoloka nyanja ya masautso; nyanja yokokoma idzagonja ndipo madzi onse a mu Nailo adzaphwa. Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha ndipo ndodo yaufumu ya Igupto idzathyoka.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 10:11
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo padziko lapansi, naphwa madzi;


Ndipo anatenga chofunda cha Eliya chidamtayikiracho, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.


Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.


nasunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asiriya, kulimbitsa manja ao mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israele.


Nyanjayo inaona, nithawa; Yordani anabwerera m'mbuyo.


Unathawanji nawe, nyanja iwe? Unabwereranji m'mbuyo, Yordani iwe?


kuti Ine ndidzathyola Aasiriya m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphewa pao.


Tsiku limenelo Ejipito adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, chifukwa cha kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pake.


Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.


Ndine amene nditi kwa nyanja yakuya, Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako;


Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa?


Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?


Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pake ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wochokera ku Ejipito, ndipo ndidzaopsa dziko la Ejipito.


Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu.


Ndipo wachisanu ndi chimodzi anatsanulira mbale yake pamtsinje waukulu Yufurate; ndi madzi ake anaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu ochokera potuluka dzuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa