Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 10:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m'dzina lake; ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m'dzina lake; ati Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ineyo ndidzalimbitsa anthu anga, ndipo adzakhala onyadira dzina la Chauta.” Ndikutero Ine Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndidzalimbitsa iwo mwa Yehova ndipo adzayenda mʼdzina lake,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 10:12
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga;


ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga.


Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m'kuwala kwa Yehova.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.


Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.


Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya.


Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.


Ndipo akalonga a Yuda adzanena m'mtima mwao, Okhala mu Yerusalemu ndiwo mphamvu yanga mu Yehova wa makamu Mulungu wao.


Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye,


Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.


ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.


Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.


Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'chisomo cha mwa Khristu Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa