Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 11:1 - Buku Lopatulika

1 Tsegula pa makomo ako Lebanoni, kuti moto uthe mikungudza yako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Tsegula pa makomo ako Lebanoni, kuti moto uthe mikungudza yako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni, kuti moto upsereze mikungudza yako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni, kuti moto unyeketse mikungudza yako!

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 11:1
14 Mawu Ofanana  

Iwe wokhala mu Lebanoni, womanga chisa chako m'mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!


Taona, Asiriya anali mkungudza wa ku Lebanoni ndi nthambi zokoma zovalira, wautali msinkhu, kunsonga kwake ndi kumitambo.


Pakuti chiwawa chidachitikira Lebanoni chidzakukuta, ndi chionongeko cha nyama chidzakuopsa; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitidwira dziko, mzinda, ndi onse okhalamo.


Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitikira dziko, mzinda, ndi onse okhalamo.


Kwerani kudziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.


Ndidzawatenganso kudziko la Ejipito, ndi kuwasonkhanitsa mu Asiriya; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Giliyadi ndi Lebanoni; koma sadzawafikira.


Chema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; chemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yotchinjirizika yagwa pansi.


Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, mu Yerusalemu.


Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa