Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 10:10 - Buku Lopatulika

10 Ndidzawatenganso kudziko la Ejipito, ndi kuwasonkhanitsa mu Asiriya; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Giliyadi ndi Lebanoni; koma sadzawafikira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndidzawatenganso kudziko la Ejipito, ndi kuwasonkhanitsa m'Asiriya; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Giliyadi ndi Lebanoni; koma sadzawafikira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ndidzaŵatulutsa ku Ejipito ndi kupita nawo kwao, ndipo ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya. Ndidzaŵafikitsa ku dziko la Giliyadi ndi la Lebanoni mpaka kudzaza dziko lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndidzawabweretsa kuchokera ku Igupto ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya. Ndidzawabwezera ku Giliyadi ndi ku Lebanoni, mpaka malo woti nʼkukhalamo adzatheratu.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 10:10
16 Mawu Ofanana  

Wamng'ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m'nthawi yake.


Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi mizinda yosakhalamo anthu.


Ndipo ndidzabwezeranso Israele kubusa lake, ndipo adzadya pa Karimele ndi pa Basani, moyo wake nudzakhuta pa mapiri a Efuremu ndi mu Giliyadi.


Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kuchokera kumadzulo.


Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Ejipito, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asiriya; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova


Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala mu Sefaradi adzakhala nayo mizinda ya kumwera, cholowa chao.


Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe.


Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo;


ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenanso ndidzakhala Mulungu wao, m'choonadi ndi m'chilungamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa