Zekariya 10:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataya konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 “Banja la Yuda ndidzalilimbitsa, banja la Yosefe ndidzalipambanitsa. Anthuwo ndidzaŵabwezanso kwao chifukwa choti ndaŵamvera chifundo. Tsono adzakhala ngati kuti sindidaŵataye, pakuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao, ndipo ndidzayankha zopempha zao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 “Ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda ndi kupulumutsa nyumba ya Yosefe. Ndidzawabwezeretsa chifukwa ndawamvera chisoni. Adzakhala ngati kuti sindinawakane, chifukwa ndine Yehova Mulungu wawo ndipo ndidzawayankha. Onani mutuwo |