Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu.
2 Samueli 22:17 - Buku Lopatulika Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga; Iye ananditulutsa m'madzi aakulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga; Iye ananditulutsa m'madzi aakulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira, ndi kundivuula m'madzi ozama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira; anandivuwula mʼmadzi ozama. |
Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu.
Tulutsani manja anu kuchokera m'mwamba; ndikwatuleni ndi kundilanditsa kumadzi aakulu, kudzanja la alendo;
Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu, pa nthawi ya kupeza Inu; indetu pakusefuka madzi aakulu sadzamfikira iye.
Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.