Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 2:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Mwana uja atakula adakampereka kwa mwana wa Farao, ndipo adasanduka mwana wake ndithu. Mwana wa Faraoyo adamutcha Mose, chifukwa adati, “Ndidamuvuula m'madzi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mwanayo atakula anakamupereka kwa mwana wa Farao ndipo anakhala mwana wake. Iye anamutcha dzina lake Mose, popeza anati, “Ndinamuvuwula mʼmadzi.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 2:10
11 Mawu Ofanana  

Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako.


Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti, chifukwa anati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha.


Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.


Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga; Iye ananditulutsa m'madzi aakulu.


Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa.


Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.


kuti akaombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana.


Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao;


Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.


Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa