Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 17:16 - Buku Lopatulika

Chifukwa chake tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti Musagona usiku uno pa madooko a kuchipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa chake tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti Musagona usiku uno pa madooko a kuchipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndiye inu tsono mutumize mau mwamsanga kwa Davide omuuza kuti asagone pa madooko a Yordani ku chipululu. Koma mwa njira iliyonse, aoloke ndithu, kuti iye pamodzi ndi anthu onse amene ali naye angagwidwe ndi kuphedwa.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsopano tumizani wamthenga msangamsanga kuti akamuwuze Davide kuti, ‘Musakagone powolokera Yorodani ku chipululu koma mukawoloke. Mukapanda kutero, mfumu ndi anthu onse amene ali naye adzaphedwa.’ ”

Onani mutuwo



2 Samueli 17:16
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mzinda ndi lupanga lakuthwa.


Ona ndidzaima pa madooko a m'chipululu kufikira afika mau ako akunditsimikizira ine.


Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abiyatara ansembewo kodi? Motero chilichonse udzachimva cha m'nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abiyatara ansembewo.


Asanene mumtima mwao, Hede, momwemo! Asanene, Tammeza iye.


Ndikadafulumira ndipulumuke kumphepo yolimba ndi namondwe.


Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse, pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.


Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.


Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.


Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.


Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake.