Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 17:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo Yonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogele; mdzakazi ankapita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m'mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo Yonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogele; mdzakazi ankapita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m'mudzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Tsono mwachizoloŵezi Yonatani ndi Ahimaazi ankadikira ku Enirogele, pafupi ndi Yerusalemu. Mdzakazi ndiye ankapita kukaŵauza zinthu, ndipo iwowo ankapita kukauza mfumu Davide. Pakuti iwowo sankayenera kuwonekera poloŵa mu mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Yonatani ndi Ahimaazi amakhala ku Eni Rogeli. Tsono wantchito wamkazi ndiye amapita kukawawuza ndipo iwo amayenera kupita kukamuwuza mfumu Davide, pakuti iwowo sankayenera kuonekera polowa mu mzinda.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 17:17
8 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? Ubwere kumzinda mumtendere pamodzi ndi ana ako aamuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.


Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abiyatara ansembewo kodi? Motero chilichonse udzachimva cha m'nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abiyatara ansembewo.


Onani, ali nao komweko ana aamuna ao awiri, Ahimaazi mwana wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiyatara; iwowa muwatumize kuti adzandiuze chilichonse mudzachimva.


Iye akali chilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abiyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino.


Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi chitsime cha Rogele, naitana abale ake onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anyamata a mfumu;


nakwera malire kunka ku Debiri, kuchokera ku chigwa cha Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa chikweza cha Adumimu, ndiko kumwera kwa mtsinje; napitirira malire kunka ku madzi a Enisemesi, ndi matulukiro ake anali ku Enirogele;


natsikira malire kunka polekezera phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha mwana wa Hinomu, ndicho cha m'chigwa cha Refaimu kumpoto; natsikira ku chigwa cha Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwera, natsikira ku Enirogele;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa