2 Samueli 15:14 - Buku Lopatulika14 Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mzinda ndi lupanga lakuthwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Ndiye Davide adauza ankhondo ake amene anali naye ku Yerusalemu kuti, “Nyamukani, tiyeni tithaŵe kuti tingasoŵe mpata wothaŵira Abisalomu. Fulumirani, kuti angatipeze mwamsanga, ndipo angatithire nkhondo ndi kutipha tonse mumzinda muno.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Ndipo Davide anati kwa akuluakulu ake amene anali mu Yerusalemu. “Bwerani! Tiyeni tithawe, mwina palibe adzapulumuke kwa Abisalomu. Tiyeni tichoke msanga, mwina iye adzabwera msanga ndi kutipitirira, nʼkuwononga ife ndi mzinda wathu ndi lupanga.” Onani mutuwo |