Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 15:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Apo nduna za mfumu zija zidauza mfumu kuti, “Amfumu, ife ankhondo anu tili okonzeka kuchita chinthu chilichonse chimene inu mungachitsimikize kuchita.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Akuluakulu a mfumu anamuyankha kuti, “Antchito anu ndi okonzeka kuchita chilichonse chimene mbuye wathu mfumu mukufuna kuchita.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:15
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mzinda ndi lupanga lakuthwa.


Mfumu nituluka, ndi banja lake lonse linamtsata. Ndipo mfumu inasiya akazi khumi ndiwo akazi aang'ono, kusunga nyumbayo.


Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzachita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.


Woyanjana ndi ambiri angodziononga; koma lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.


Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.


Ndipo wonyamula zida zake anena naye, Chitani zonse zili mumtima mwanu; palukani, onani ndili pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa