Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 5:4 - Buku Lopatulika

4 Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ife amene tili mu msasa uno timalemedwa ndipo timabuula. Sitifuna kuuvula msasawu ai, koma kwenikweni tikadakonda kuvala nyumba ija ya Kumwamba pamwamba pake, kuti chimene chili chakufa chimizidwe ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Pamene tili mu msasa uno, timalemedwa ndipo timabuwula, chifukwa sitifuna kukhala amaliseche koma ovala nyumba yathu ya kumwamba, kuti chimene chili chakufa chimezedwe ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 5:4
8 Mawu Ofanana  

Iye wameza imfa kunthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa padziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.


Pokhala panga pachotsedwa, pandisunthikira monga hema wa mbusa; Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba; Iye adzandidula ine poomberapo; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.


Ndipo si chotero chokha, koma ife tomwe, tili nazo zipatso zoyamba za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo chiomboledwe cha thupi lathu.


Taonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,


Pakutinso m'menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera Kumwamba;


ngatitu povekedwa sitidzapezedwa amaliseche.


Ndipo ndichiyesa chokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa