Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simei chifukwa cha kutemberera wodzozedwa wa Yehova?
2 Samueli 16:9 - Buku Lopatulika Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Abisai, mwana wa Zeruya, adafunsa mfumu kuti, “Bwanji mukulola galu wakufayu kuti akutukwaneni chotere, inu mbuyanga mfumu? Mundilole ndikamdule pa khosi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.” |
Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simei chifukwa cha kutemberera wodzozedwa wa Yehova?
Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa mu Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero?
Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo.
Pomwepo Abinere anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa galu wa Yuda kodi? Lero lino ndilikuchitira zokoma nyumba ya Saulo atate wanu, ndi abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindinakuperekani m'dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu.
Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya galu wakufa monga ine.
Ndipo pamene ophunzira ake Yakobo ndi Yohane anaona, anati, Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo?
Ndipo Paulo anati, Sindinadziwe, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.
Nanga mfumu ya Israele inatulukira yani; inu mulikupirikitsa yani? Galu wakufa, kapena nsabwe.