Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 16:8 - Buku Lopatulika

8 Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Saulo, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwake; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, chifukwa uli munthu wa mwazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Saulo, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwake; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, chifukwa uli munthu wa mwazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chauta wakulipsira chifukwa chakuti udapha onse a banja la Saulo, nulanda ufumu wake. Ndipotu Chauta wapereka ufumuwo kwa mwana wako Abisalomu. Ona, kutha kwako nkumeneku, pakuti iweyo ndiwe wopha anthu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Yehova wakubwezera chifukwa cha magazi onse amene unakhetsa pa nyumba ya Sauli, yemwe iwe ukulamulira mʼmalo mwake. Yehova wapereka ufumu kwa mwana wako Abisalomu. Ndipo ona mathero ako ndi amenewa chifukwa ndiwe munthu wopha anthu!”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 16:8
18 Mawu Ofanana  

Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.


Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka ku Yerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu.


Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simei chifukwa cha kutemberera wodzozedwa wa Yehova?


Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.


niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele.


Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga.


Ambiri amati kwa moyo wanga, alibe chipulumutso mwa Mulungu.


Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti? Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?


chifukwa cha mau a mdani, chifukwa cha kundipsinja woipa; pakuti andisenza zopanda pake, ndipo adana nane mumkwiyo.


ngati ndambwezera choipa iye woyanjana ndine; (inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda chifukwa);


Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.


popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.


kuti chiwawa adachitira ana aamuna makumi asanu ndi awiri a Yerubaala chimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ake a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ake, awaphe abale ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa