2 Samueli 3:8 - Buku Lopatulika8 Pomwepo Abinere anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa galu wa Yuda kodi? Lero lino ndilikuchitira zokoma nyumba ya Saulo atate wanu, ndi abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindinakuperekani m'dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Pomwepo Abinere anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa galu wa Yuda kodi? Lero lino ndilikuchitira zokoma nyumba ya Saulo atate wanu, ndi abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindinakuperekani m'dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Abinere adapsa nawo mtima kwambiri mau a Isiboseti, ndipo adati, “Kodi ukundiyesa ine galu wa Ayuda, adani athu? Kuyambira poyamba pomwe ndakhala wokhulupirika kwa Saulo bambo wako, abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindidakupereke m'manja mwa Davide. Ndiye lero, iwe ukundiimba mlandu woti ndachimwa ndi mkazi! Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Abineri anakwiya kwambiri chifukwa cha zimene Isi-Boseti ananena ndipo anamuyankha kuti “Kodi ukuyesa ndine mutu wagalu umene ali mbali ya Ayuda? Lero lino ndine wokhulupirika ku nyumba ya abambo ako, Sauli ndi banja lake ndi anzake. Ine sindinakupereke kwa Davide, koma tsopano ukundinena pa cholakwa chimene ndachita pa mkazi uyu! Onani mutuwo |