Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 3:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Abineri anakwiya kwambiri chifukwa cha zimene Isi-Boseti ananena ndipo anamuyankha kuti “Kodi ukuyesa ndine mutu wagalu umene ali mbali ya Ayuda? Lero lino ndine wokhulupirika ku nyumba ya abambo ako, Sauli ndi banja lake ndi anzake. Ine sindinakupereke kwa Davide, koma tsopano ukundinena pa cholakwa chimene ndachita pa mkazi uyu!

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Pomwepo Abinere anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa galu wa Yuda kodi? Lero lino ndilikuchitira zokoma nyumba ya Saulo atate wanu, ndi abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindinakuperekani m'dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pomwepo Abinere anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa galu wa Yuda kodi? Lero lino ndilikuchitira zokoma nyumba ya Saulo atate wanu, ndi abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindinakuperekani m'dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Abinere adapsa nawo mtima kwambiri mau a Isiboseti, ndipo adati, “Kodi ukundiyesa ine galu wa Ayuda, adani athu? Kuyambira poyamba pomwe ndakhala wokhulupirika kwa Saulo bambo wako, abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindidakupereke m'manja mwa Davide. Ndiye lero, iwe ukundiimba mlandu woti ndachimwa ndi mkazi!

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 3:8
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.”


Pa nthawi imeneyi Abineri mwana wa Neri, wolamulira ankhondo a Sauli, anatenga Isi-Boseti mwana wa Sauli ndi kubwera naye ku Mahanaimu.


Tsopano chitani zimenezo! Pakuti Yehova analonjeza Davide kuti, ‘Kudzera mwa mtumiki wanga Davide ndidzapulumutsa anthu anga Aisraeli mʼdzanja la Afilisti ndi kuwachotsa mʼmanja mwa adani awo.’ ”


Mulungu andilange ine Abineri, andilange kwambiri, ngati sindichitira Davide zimene Yehova anamulonjeza iye mwa lumbiro.


Kale lija, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova anakuwuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”


Mefiboseti anawerama pansi ndipo anati, “Mtumiki wanu ndine yani kuti musamale galu wakufa ngati ine?”


Ndipo Hazaeli anati, “Kodi kapolo wanune, amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita chinthu chachikulu chotere?” Elisa anayankha kuti, “Yehova wandionetsa kuti iwe udzakhala mfumu ya ku Aramu.”


Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.


Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira ndani? Kodi iwe wafuwulira ndi kumuyangʼana monyada ndani? Watsutsana ndi Woyerayo wa Israeli!


Musabweretse malipiro a wachiwerewere wamkazi kapena wamwamuna Mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kudzapereka za malumbiro aliwonse, chifukwa Yehova Mulungu wanu amadana ndi zimenezi.


Samueli anati kwa iye, “Yehova wangʼamba ufumu wanu kuchoka kwa inu, ndipo waupereka kwa mnzanu woposa inu.


Iye anati kwa Davide, “Kodi ndine galu, kuti ubwere kwa ine ndi ndodo?” Ndipo Mfilisitiyo anamutemberera Davide potchula mayina a milungu yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa