Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 23:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Paulo anati, Sindinadziwe, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Paulo anati, Sindinadziwa, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Paulo adati, “Pepani abale, sindimadziŵa kuti ndi mkulu wa ansembe onse. Paja mau a Mulungu akuti, ‘Usamnenere zoipa woweruza anthu ako.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Paulo anayankha nati, “Abale, ine sindinazindikire kuti ndi mkulu wa ansembe; pakuti kunalembedwa kuti, ‘Usayankhule zoyipa kwa mtsogoleri wa anthu ako.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 23:5
6 Mawu Ofanana  

Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako.


Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo.


Ndipo iwo akuimirirako anati, Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu?


Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;


koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa