2 Samueli 16:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.” Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Pamenepo Abisai, mwana wa Zeruya, adafunsa mfumu kuti, “Bwanji mukulola galu wakufayu kuti akutukwaneni chotere, inu mbuyanga mfumu? Mundilole ndikamdule pa khosi.” Onani mutuwo |
Abineri anakwiya kwambiri chifukwa cha zimene Isi-Boseti ananena ndipo anamuyankha kuti “Kodi ukuyesa ndine mutu wagalu umene ali mbali ya Ayuda? Lero lino ndine wokhulupirika ku nyumba ya abambo ako, Sauli ndi banja lake ndi anzake. Ine sindinakupereke kwa Davide, koma tsopano ukundinena pa cholakwa chimene ndachita pa mkazi uyu!