Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 15:30 - Buku Lopatulika

Ndipo Davide anakwera pa chikweza cha ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anafunda mutu wake nayenda ndi mapazi osavala; ndi anthu onse amene anali naye anafunda munthu yense mutu wake ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Davide anakwera pa chikweza cha ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anafunda mutu wake nayenda ndi mapazi osavala; ndi anthu onse amene anali naye anafunda munthu yense mutu wake ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Davide adakwera phiri la Olivi, akunka nalira, osavala kanthu kuphazi, atafundira kumutu. Anthu onse amene anali naye adafundanso kumutu, ndipo nawonso adakwera phiri akunka nalira.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma Davide anapitirira ndi kukakwera phiri la Olivi akupita nalira. Anafunda kumutu koma sanavale nsapato. Anthu onse amene anali naye anafundanso kumutu, ndipo nawonso amalira pamene amapita.

Onani mutuwo



2 Samueli 15:30
21 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake Zadoki ndi Abiyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko.


Ndipo mfumu inafunda nkhope yake, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana.


Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu aang'ono;


Ndipo Mordekai anabweranso kuchipata cha mfumu. Koma Hamani anafulumira kunka kwao, wachisoni ndi wofunda mutu wake.


Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.


Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire chilemba, nuvale nsapato kumapazi ako, usaphimbe milomo yako. Kapena kudya mkate wa anthu.


Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu kumapazi anu, simudzachita chisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzake.


Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.


Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.


Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, paphiri lotchedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira,


Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;


Ndipo m'mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira,


Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa mu Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona paphiri lotchedwa la Azitona.


Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye.


Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kuchokera kuphiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata.


Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.


Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.