Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 22:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Pambuyo pake Yesu adatuluka mu mzinda napita ku Phiri la Olivi monga adaazoloŵera. Ndipo ophunzira ake adapita naye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Yesu anapitanso monga mwa masiku onse ku Phiri la Olivi, ndipo ophunzira ake anamutsatira Iye.

Onani mutuwo Koperani




Luka 22:39
10 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,


Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona.


Ndipo Iye analowa mu Yerusalemu, mu Kachisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.


Ndipo masiku onse madzulo anatuluka Iye m'mzinda.


Ndipo pamene anakhala Iye paphiri la Azitona, popenyana ndi Kachisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andrea, kuti,


Ndipo ataimba nyimbo, anatuluka, namuka kuphiri la Azitona.


Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa mu Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona paphiri lotchedwa la Azitona.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa