Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 21:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa mu Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona paphiri lotchedwa la Azitona.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa m'Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona pa phiri lotchedwa la Azitona.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Masiku onse Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, koma usiku ankatuluka kukakhala ku phiri lotchedwa Phiri la Olivi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Tsiku lililonse Yesu amaphunzitsa ku Nyumba ya Mulungu, ndi madzulo ali wonse Iye amachoka kukakhala pa phiri la Olivi usiku wonse.

Onani mutuwo Koperani




Luka 21:37
15 Mawu Ofanana  

Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.


Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,


Ndipo Iye anawasiya, natuluka m'mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko.


Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona.


Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.


Ndipo m'mawa mwake, atatuluka ku Betaniya, Iye anamva njala.


Ndipo masiku onse madzulo anatuluka Iye m'mzinda.


Masiku onse ndinali nanu mu Kachisi ndilikuphunzitsa, ndipo simunandigwire Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwaniritsidwe.


Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, paphiri lotchedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira,


Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;


Ndipo analikuphunzitsa mu Kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga Iye;


Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye.


Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.


Koma Yudasinso amene akampereka Iye, anadziwa malowa; chifukwa Yesu akankako kawirikawiri ndi ophunzira ake.


Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kuchokera kuphiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa