Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 15:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Kenaka Davide adamva kuti Ahitofele ali pakati pa anthu ogalukira, pamodzi ndi Abisalomu. Tsono Davideyo adayamba kupemphera, adati, “Ine Chauta ndikukupemphani, musandutse uphungu wa Ahitofele kuti ukhale uchitsiru.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Tsono Davide anamva kuti, “Ahitofele ali pakati pa anthu owukira pamodzi ndi Abisalomu.” Choncho Davide anapemphera, “Inu Yehova, musandutse uphungu wa Ahitofele ukhale uchitsiru.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:31
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.


Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.


Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Pomwepo Abisalomu anati, Kaitane tsopano Husai Mwariki yemwe, timvenso chimene anene iye.


Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofele suli wabwino.


Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera, kuti manja ao sangathe kuchita chopangana chao.


Ndipo anandizinga ndi mau a udani, nalimbana nane kopanda chifukwa.


Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine! Akundiukira ine ndi ambiri.


Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.


Izizo ziuzungulira pa malinga ake usana ndi usiku; ndipo m'kati mwake muli zopanda pake ndi chovuta.


Pakuti si mdani amene ananditonzayo; pakadatero ndikadachilola, amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida; pakadatero ndikadambisalira:


Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.


Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:


Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.


Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitse nzeru ya dziko lapansi?


Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa