Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 19:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, paphiri lotchedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri lotchedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Atafika pafupi ndi midzi ya Betefage ndi Betaniya, pafupi ndi phiri lotchedwa Phiri la Olivi, adatuma ophunzira aŵiri,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Iye atayandikira ku Betifage ndi Betaniya pa phiri lotchedwa Olivi, Iye anatuma awiri a ophunzira nati kwa iwo,

Onani mutuwo Koperani




Luka 19:29
11 Mawu Ofanana  

Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.


Ndipo Iye anawasiya, natuluka m'mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko.


nati, Mukani kumudzi uli pandunji panu; m'menemo, polowa, mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, pamenepo palibe munthu anakwerapo nthawi iliyonse; mummasule iye nimumtenge.


Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake paphiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau aakulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;


Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa mu Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona paphiri lotchedwa la Azitona.


Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye.


Ndipo anatuluka nao kufikira ku Betaniya; nakweza manja ake, nawadalitsa.


Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kuchokera kuphiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa