Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 11:2 - Buku Lopatulika

Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zidangochitika kuti tsiku lina chakumadzulo, Davide adadzuka pabedi pake, namayenda pamwamba pa denga la nyumba yake yaufumu. Ali padengapo, adaona mkazi wina akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwabasi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri.

Onani mutuwo



2 Samueli 11:2
28 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene anayandikira kulowa mu Ejipito, anati kwa Sarai mkazi wake, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako;


Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso.


Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.


Ndipo iye anasiya zake zonse m'manja a Yosefe: osadziwa chomwe anali nacho, koma chakudya chimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.


kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.


Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye.


Ndipo kwa Abisalomu kunabadwa ana aamuna atatu ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake ndiye Tamara, iye ndiye mkazi wokongola nkhope.


Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika kunyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana.


Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali chigonere pakama pake m'chipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wake, nautenga namuka njira ya kuchidikha usiku wonse.


Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?


Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.


Ulesi ugonetsa tulo tofa nato; ndipo moyo wamkhongono udzamva njala.


Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.


Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake.


alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo, ndi kuyenda panjira ya kunyumba yake;


ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.


Chimene ndikuuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m'khutu, muchilalikire pa matsindwi a nyumba.


iye ali pamwamba pa tsindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwake;


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.


Koma m'mawa mwake, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mzinda, Petro anakwera patsindwi kukapemphera, ngati pa ora lachisanu ndi chimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;


Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.


Usasirire mkazi wake wa mnzako; usakhumbe nyumba yake ya mnzako, munda wake, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.


Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.


Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumzinda, iye anakamba ndi Saulo pamwamba pa nyumba yake.