Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 4:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika kunyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika kunyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Rekabu ndi Baana, ana aja a Rimoni Mbeerotiŵa, adanyamuka. Masana dzuŵa likuswa mtengo, adakafika ku nyumba ya Isiboseti, nthaŵi imene iyeyo anali pa mpumulo wamasana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Choncho Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti ananyamuka kupita ku nyumba ya Isi-Boseti, ndipo anafika nthawi ya masana kukutentha pamene iye amapumula.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 4:5
9 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.


Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;


Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;


Ndipo mnyamata wake Zimiri, ndiye woyang'anira dera lina la magaleta ake, anampangira chiwembu; koma iye anali mu Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba mu Tiriza.


Ndipo atamchokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikulu), anyamata ake anamchitira chiwembu, chifukwa cha mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pake, namwalira iye; ndipo anamuika m'mzinda wa Davide, koma osamuika m'manda a mafumu.


Ndipo chipatukire Amaziya kusatsata Yehova, namchitira chiwembu mu Yerusalemu, nathawira ku Lakisi iyeyu; koma anatuma omtsatira ku Lakisi, namupha komweko.


Ndipo anyamata ake anampangira chiwembu, namupha m'nyumba yakeyake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa