2 Samueli 4:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwake; ndi Rekabu ndi Baana mbale wake anathawa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwake; ndi Rekabu ndi Baana mbale wake anathawa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Mkazi wolonda pa khomo la nyumbayo ankapuntha tirigu, kenaka nkuyamba kuwodzera, nagona. Choncho Rekabu ndi Baana mbale wake adangoti kwakwalala kuloŵa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Iwo analowa mʼchipinda chamʼkati ngati kuti amakatenga tirigu, ndipo anamulasa mʼmimba. Kenaka Rekabu ndi mʼbale wake Baana anathawa. Onani mutuwo |