Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 4:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iwo analowa mʼchipinda chamʼkati ngati kuti amakatenga tirigu, ndipo anamulasa mʼmimba. Kenaka Rekabu ndi mʼbale wake Baana anathawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwake; ndi Rekabu ndi Baana mbale wake anathawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwake; ndi Rekabu ndi Baana mbale wake anathawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mkazi wolonda pa khomo la nyumbayo ankapuntha tirigu, kenaka nkuyamba kuwodzera, nagona. Choncho Rekabu ndi Baana mbale wake adangoti kwakwalala kuloŵa.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 4:6
5 Mawu Ofanana  

Koma iye anakana kuleka kumuthamangitsa. Choncho Abineri anabaya Asaheli mʼmimba ndi msonga ya mkondo wake ndipo mkondowo unatulukira mbali ina. Iye anagwa ndi kufera pamalo pomwepo. Ndipo munthu aliyense amayima akafika pamalo pamene anagwera ndi kufa.


Amasa sanayangʼanitsitse lupanga limene linali mʼdzanja la Yowabu, ndipo Yowabu anamubaya nalo mʼmimba ndipo matumbo ake anatuluka ndi kugwera pansi. Popanda kubayanso kachiwiri, Amasa anafa. Ndipo Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anathamangitsa Seba mwana wa Bikiri.


Tsono Abineri atabwerera ku Hebroni, Yowabu anamutengera pambali ku chipata, kukhala ngati akufuna kuyankhula naye mwamseri. Ndipo kumeneko pobwezera imfa ya mʼbale wake Asaheli, Yowabu analasa iyeyo mʼmimba, ndipo anafa.


Koma Isiboseti anali ndi anthu akuluakulu awiri amene ankatsogolera magulu a ankhondo. Mmodzi mwa iwo dzina lake linali Baana ndipo mnzakeyo anali Rekabu. Iwo anali ana a Rimoni wa banja la Beeroti wa fuko la Benjamini Beeroti. Iwo ankatengedwa ngati mbali imodzi ya Benjamini,


Ehudi anathawa pamene iwo ankadikira. Iye anadzera ku malo a miyala yozokotedwa kuja ndi kuthawa kupita ku Seiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa