2 Samueli 4:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Yonatani, mwana wa Saulo, anali ndi mwana wake wolumala miyendo, dzina lake Mefiboseti. Ndiye kuti mwanayo ali wa zaka zisanu, mbiri ya imfa ya Saulo ndi Yonatani idamveka ku Yezireele. Tsono mlezi wake wa mwanayo atamva, adamtenga mwana uja, nkuyamba kuthaŵa. Ndiye pothaŵa mofulumira choncho, mwanayo adampulumuka, nagwa pansi, nkuvulala. Kulumala kunali komweko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 (Yonatani mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna amene anali wolumala mapazi ake onse awiri. Iye anali ndi zaka zisanu pamene nkhani ya Sauli ndi Yonatani inamveka kuchokera ku Yezireeli. Amene amamulera anamunyamula ndi kuthawa naye, koma pamene amachita zinthu mofulumira mwanayo anagwa ndipo analumala. Dzina lake linali Mefiboseti). Onani mutuwo |