Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 4:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 (Yonatani mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna amene anali wolumala mapazi ake onse awiri. Iye anali ndi zaka zisanu pamene nkhani ya Sauli ndi Yonatani inamveka kuchokera ku Yezireeli. Amene amamulera anamunyamula ndi kuthawa naye, koma pamene amachita zinthu mofulumira mwanayo anagwa ndipo analumala. Dzina lake linali Mefiboseti).

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Yonatani, mwana wa Saulo, anali ndi mwana wake wolumala miyendo, dzina lake Mefiboseti. Ndiye kuti mwanayo ali wa zaka zisanu, mbiri ya imfa ya Saulo ndi Yonatani idamveka ku Yezireele. Tsono mlezi wake wa mwanayo atamva, adamtenga mwana uja, nkuyamba kuthaŵa. Ndiye pothaŵa mofulumira choncho, mwanayo adampulumuka, nagwa pansi, nkuvulala. Kulumala kunali komweko.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 4:4
10 Mawu Ofanana  

Koma mfumu inasunga Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha kulumbira kumene mfumu Davide ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pamaso pa Yehova.


Ndipo Mefiboseti anakhala mu Yerusalemu chifukwa nthawi zonse amadya ndi mfumu. Iye anali wolumala mapazi ake onse.


Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?” Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.”


Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye. Davide anati, “Mefiboseti!” Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”


Koma Hadadi akanali mwana anathawira ku Igupto pamodzi ndi akuluakulu ena a ku Edomu amene ankatumikira abambo ake.


Mwana wa Yonatani anali Meri-Baala, amene anabereka Mika.


Mwana wa Yonatani anali Meri-Baala, amene anabereka Mika.


Afilisti anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, ndipo Israeli anamanga misasa yawo pa chitsime cha Yezireeli.


Choncho Davide ndi anthu ake anadzuka mmamawa kubwerera ku dziko la Afilisti. Koma Afilistiwo anapita ku Yezireeli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa