Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 12:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo panali pamene anayandikira kulowa mu Ejipito, anati kwa Sarai mkazi wake, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo panali pamene anayandikira kulowa m'Ejipito, anati kwa Sarai mkazi wake, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pamene anali pafupi kuwoloka malire a Ejipito, adauza mkazi wake Sarai kuti, “Ndikudziŵa kuti iwetu ndiwe mkazi wokongola.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Atatsala pangʼono kulowa mu Igupto, Abramu anamuwuza mkazi wake Sarai kuti, “Ndimadziwa kuti ndiwe mkazi wokongola kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 12:11
14 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene Abramu analowa mu Ejipito, Aejipito anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri.


Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga.


Ndipo Abrahamu anati za Sara mkazi wake, Iye ndiye mlongo wanga: ndipo Abimeleki mfumu ya Gerari anatumiza namtenga Sara


Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m'maonekedwe ake, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera.


ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.


Maso a Leya anali ofooka, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola.


kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.


Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.


Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwe.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.


Wokondedwa wanga ali kwa ine ngati chipukutu cha maluwa ofiira m'minda yamipesa ya ku Engedi.


Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa