Genesis 3:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono mkaziyo adaona kuti mtengowo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako mwamuna wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso. Onani mutuwo |