Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
2 Akorinto 3:5 - Buku Lopatulika si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti mwa ife tokha mulibe kanthu kamene kangatiganizitse kuti tingathe kuchita ntchitoyi patokha. Amene amatipatsa mphamvu ndi Mulungu kuti tithe kuichita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu. |
Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova.
Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.
Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mzinda muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba.
Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito,
Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.
Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo.
Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;
pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.