1 Akorinto 15:10 - Buku Lopatulika10 Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhala chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Koma chifukwa chakuti Mulungu adandikomera mtima, ndili monga ndilirimu. Ndipo kukoma mtima kwakeko sikunali kopanda phindu, popeza kuti ndidagwira ntchito koposa atumwi ena onse. Komabe si ndine ndidaigwira, koma mphamvu za Mulungu zimene zikundilimbikitsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Koma mwachisomo cha Mulungu, ndili mmene ndililimu, ndipo chisomo chake kwa ine sichinali chopanda ntchito. Ndinagwira ntchito kuposa ena onse a iwo. Choncho sindine koma chisomo cha Mulungu chimene chinali ndi ine. Onani mutuwo |