Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.
2 Akorinto 13:7 - Buku Lopatulika Ndipo tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke ovomerezeka, koma kuti inu mukachite chabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke ovomerezeka, koma kuti inu mukachite chabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tikupempha Mulungu kuti musachite choipa chilichonse. Osati kuti ife tiwoneke ngati opambana, koma kuti inu muchite zimene zili zoyenera, ngakhale ife tiwoneke ngati talephera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musadzachite kanthu kena kalikonse kolakwa. Osati chifukwa choti anthu aone kuti ife tapambana mayesowo koma kuti mudzachite zokhoza ngakhale anthu atamationa ngati olephera. |
Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.
Sindipempha kuti muwachotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.
Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;
Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.
Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.
Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo ovomerezedwa aonetsedwe mwa inu.
Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.
Pakuti tikondwera, pamene ife tifooka ndi inu muli amphamvu; ichinso tipempherera, ndicho ungwiro wanu.
koma m'zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.
Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.
ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.