Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 10:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti, akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Paja ena amati, “Makalata a Paulo ngaukali ndi amphamvu, koma mwiniwake akakhala pakati pathu, iyeyo ngwofooka ndipo mau ake ndi achabe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pakuti ena amati, “Makalata ake ndi awukali ndi amphamvu koma maonekedwe a thupi lake ndi wosagwira mtima ndipo mayankhulidwe ake ndi achabechabe.”

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 10:10
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.


Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana.


Pakuti Khristu sananditume ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.


Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziwe Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira.


Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;


Woteroyo ayese ichi kuti monga tili ife ndi mau mwa makalata, pokhala palibe ife, tili oterenso m'machitidwe pokhala tili pomwepo.


kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa makalatawo.


Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.


Ndipo ndingakhale ndili wosaphunzira m'manenedwe, koma sinditero m'chidziwitso, koma m'zonse tachionetsa kwa inu mwa anthu onse.


popeza mufuna chitsimikizo, cha Khristu wakulankhula mwa ine; amene safooka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa