ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.
2 Akorinto 1:3 - Buku Lopatulika Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. |
ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.
Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.
Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.
nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.
Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; nakwezeke Mulungu wa chipulumutso changa.
Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.
Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.
Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima mu Yerusalemu.
Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo;
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.
Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama.
Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito;
kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;
Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m'choonadi, monga tinalandira lamulo lochokera kwa Atate.
Yense wakupitirira, wosakhala m'chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m'chiphunzitso, iyeyo ali nao Atate ndi Mwana.