Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 4:34 - Buku Lopatulika

34 Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo;

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Pomaliza pa zaka zimenezo ine, Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndipo nzeru zanga zinabwereramo. Kenaka ndinatamanda Wammwambamwamba; ndinamupatsa ulemu ndi kumulemekeza Iye amene akhala nthawi zonse. Ulamuliro wake ndi ulamuliro wa nthawi zonse; ufumu wake udzakhala ku mibadomibado.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 4:34
57 Mawu Ofanana  

Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.


Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.


Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.


nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.


Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya; aonongeka amitundu m'dziko lake.


Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga: Zaka zanu zikhalira m'mibadwomibadwo.


Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!


Ndipo apereke nsembe zachiyamiko, nafotokozere ntchito zake ndi kufuula mokondwera.


Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!


Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!


Ntchito za manja ake ndizo choonadi ndi chiweruzo; malangizo ake onse ndiwo okhulupirika.


Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti?


Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba.


Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse.


Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya.


Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko; numchitire Wam'mwambamwamba chowinda chako.


Achita ufumu mwa mphamvu yake kosatha; maso ake ayang'anira amitundu; opikisana ndi Iye asadzikuze.


Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake; ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba.


Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.


Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.


Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa.


Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.


Chifukwa chake lemekezani inu Yehova kum'mawa, ngakhale dzina la Yehova, Mulungu wa Israele, m'zisumbu za m'nyanja.


Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.


Kodi m'kamwa mwa Wam'mwambamwamba simutuluka zovuta ndi zabwino?


Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.


Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.


Chandikomera kuonetsa zizindikiro ndi zozizwa, zimene anandichitira Mulungu Wam'mwambamwamba.


Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukadzatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira.


Ha! Zizindikiro zake nzazikulu, ndi zozizwa zake nza mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwake ku mibadwomibadwo.


Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; ndipo zidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.


Nthawi yomweyi nzeru zanga zinandibwerera, ndi chifumu changa ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uonekenso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akulu anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika mu ufumu wanga, Iye nandionjezeranso ukulu wochuluka.


Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;


ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama zakuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.


Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro.


Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.


Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu a opatulika a Wam'mwambamwamba; ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzamtumikira ndi kummvera.


Chifukwa chake Yehova wakhala maso pa choipacho, ndi kutifikitsira icho; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu ntchito zake zonse azichita; ndipo sitinamvere mau ake.


Pamenepo anafuulira kwa Yehova, nati, Tikupemphanitu, Yehova, tisatayike chifukwa cha moyo wa munthu uyu, musatisenzetse mwazi wosachimwa; pakuti, Inu Yehova, mwachita monga mudakomera Inu.


ndipo wotsimphinayo ndidzamuyesa wotsala, ndi iye wotayidwa kutali mtundu wamphamvu; ndipo Yehova adzakhala mfumu yao m'phiri la Ziyoni kuyambira pamenepo kufikira kosatha.


ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo kunthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.


Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.


Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha;


Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.


Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.


amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.


nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo kunthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu zili momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu zili momwemo, ndi nyanja ndi zinthu zili momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,


Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, kwa Iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa