Danieli 4:33 - Buku Lopatulika33 Nthawi yomweyo anachitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumchotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng'ombe iye, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lake lidamera ngati nthenga za chiombankhanga ndi makadabo ake ngati makadabo a mbalame. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201433 Nthawi yomweyo anachitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumchotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng'ombe iye, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lake lidamera ngati nthenga za chiombankhanga ndi makadabo ake ngati makadabo a mbalame. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero33 Nthawi yomweyo zonse zimene zinanenedwa zokhudza Nebukadinezara zinakwaniritsidwa. Iye anachotsedwa pakati pa anthu ndipo ankadya udzu ngati ngʼombe. Thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba mpaka tsitsi lake linakula ngati nthenga za chiwombankhanga ndi zikhadabo ngati zikhadabo za mbalame. Onani mutuwo |
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.
ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama zakuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.