Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Yohane 1:4 - Buku Lopatulika

4 Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m'choonadi, monga tinalandira lamulo lochokera kwa Atate.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m'choonadi, monga tinalandira lamulo lochokera kwa Atate.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndidakondwera kwambiri kuti ndidapeza ana anu ena akuyenda motsata choona, monga Atate adatilamulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndinakondwera kwambiri nditapeza ana anu ena akuyenda mʼchoonadi, monga Atate anatilamulira.

Onani mutuwo Koperani




2 Yohane 1:4
12 Mawu Ofanana  

Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.


Chilamulo cha zoona chinali m'kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeke m'milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu.


sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi;


Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukakamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,


Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo.


iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa