Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Yohane 1:3 - Buku Lopatulika

3 Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, m'choonadi ndi m'chikondi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, m'choonadi ndi m'chikondi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mulungu Atate ndi Yesu Khristu, Mwana wa Atate, atikomere mtima ndi kutipatsa chifundo ndi mtendere m'choona ndi m'chikondi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Yesu Khristu, Mwana wa Atate, zikhale ndi ife mʼchoonadi ndi mʼchikondi.

Onani mutuwo Koperani




2 Yohane 1:3
9 Mawu Ofanana  

Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.


kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.


koma chisomo cha Ambuye wathu chidachulukatu pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.


kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.


Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.


Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.


Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikondana nao m'choonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira choonadi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa