1 Samueli 7:16 - Buku Lopatulika Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m'malo onse amenewa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m'malo onse amenewa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chaka ndi chaka ankapanga ulendo wozungulira, kupita ku Betele, Giligala ndi ku Mizipa, ndipo ankaweruza milandu ku malo onseŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chaka ndi chaka Samueli ankakonza ulendo wozungulira kuchokera ku Beteli mpaka ku Giligala ndi Mizipa, kuweruza milandu ya Aisraeli mʼmadera onsewa. |
Ndipo Yakobo anafika ku Luzi, ndiko ku dziko la Kanani (ndiwo Betele), iye ndi anthu onse anali pamodzi ndi iye.
Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.
koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.
Ndipo ana a Israele anamanga misasa ku Giligala; nachita Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, madzulo, m'zidikha za Yeriko.
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndakukunkhunizirani mtonzo wa Ejipito. Chifukwa chake dzina la malowo analitcha Giligala kufikira lero lino.
Ndipo anali nao ana aamuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo mizinda makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi.
Ndipo anali nao ana aamuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu.
Inu akuyenda okwera pa abulu oyera, inu akukhala poweruzira, ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani.
Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Tiyeni tipite ku Giligala, kukonzanso ufumu kumeneko.
Ndipo Samuele anati, Musonkhanitse Aisraele onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.