Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 10:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anali nao ana aamuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo mizinda makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo midzi makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Iyeyu anali nawo ana makumi atatu amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Anawo anali nayonso mizinda makumi atatu imene mpaka pano ikutchedwa Havoti-Yairo m'dziko la Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu, amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Iwo anali ndi mizinda makumi atatu mʼdziko la Giliyadi, imene mpaka lero ikutchedwa kuti Havoti Yairi.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 10:4
8 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko.


Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.


Ndipo Yairi mwana wa Manase ananka nalanda midzi yao, naitcha Havoti-Yairi.


Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino).


Atafa iye, anauka Yairi Mgiliyadi, naweruza Israele zaka makumi awiri mphambu ziwiri.


Nafa Yairi, naikidwa mu Kamoni.


Ndipo anali nao ana aamuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu.


Inu akuyenda okwera pa abulu oyera, inu akukhala poweruzira, ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa