Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 23:12 - Buku Lopatulika

Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Davide adafunsanso kuti, “Kodi anthu a ku Keila adzandipereka ine ndi anthu anga kwa Saulo?” Chauta adati, “Inde adzakupereka.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Davide anafunsanso, “Kodi anthu a ku Keila adzapereka ine ndi anthu angawa kwa Sauli?” Ndipo Yehova anayankha, “Iwo adzakuperekanidi.”

Onani mutuwo



1 Samueli 23:12
12 Mawu Ofanana  

Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira munthu.


Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.


Ndipo simunandipereke m'dzanja la mdani; munapondetsa mapazi anga pali malo.


Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye.


Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?


Ndipo Yehova anandidziwitsa, ndipo ndinadziwa; ndipo wandisonyeza ine machitidwe ao.


Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.


Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera chifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samisoni, kumchitira iye monga anatichitira ife.


Kodi amuna a ku Keila adzandipereka m'dzanja lake? Kodi Saulo adzatsikira ndithu, monga mnyamata wanu wamva? Yehova Mulungu wa Israele, ndikupemphani, muuze mnyamata wanu. Ndipo Yehova anati, Adzatsika.


Chifukwa chake mfumu, tsikani, monga umo mukhumbire m'mtima mwanu kutsika; ndipo kudzakhala kwathu kumpereka iye m'dzanja la mfumu.


Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.