Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 23:20 - Buku Lopatulika

20 Chifukwa chake mfumu, tsikani, monga umo mukhumbire m'mtima mwanu kutsika; ndipo kudzakhala kwathu kumpereka iye m'dzanja la mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Chifukwa chake mfumu, tsikani, monga umo mukhumbire m'mtima mwanu kutsika; ndipo kudzakhala kwathu kumpereka iye m'dzanja la mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Tsono inu amfumu, ife tadziŵa kuti mukumfunafuna kwambiri, choncho bwerani ndithu. Ifeyo tidzampereka kwa inu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Tsopano inu, mubwere nthawi iliyonse imene mukufuna, ndipo ife tidzamupereka kwa mfumu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 23:20
11 Mawu Ofanana  

Pomwepo Abinere anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisraele onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Chomwecho Davide analawirana ndi Abinere, namuka iye mumtendere.


Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.


Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.


Chifuniro cha olungama chifikitsa zabwino zokha; koma chiyembekezo cha oipa mkwiyo.


Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo.


Ambiri afunafuna chiyanjano cha mkulu; koma chiweruzo cha munthu chichokera kwa Yehova.


Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina mu Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha;


Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.


Saulo nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; chifukwa munandichitira ine chifundo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa