Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 23:21 - Buku Lopatulika

21 Saulo nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; chifukwa munandichitira ine chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Saulo nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; chifukwa munandichitira ine chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Apo Saulo adati, “Chauta akudalitseni, pakuti mwandikomera mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Sauli anayankha kuti, “Yehova akudalitseni pakuti mwandichitira chifundo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 23:21
9 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga.


Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Saulo, ndi kumuika.


Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.


Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.


Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.


Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga.


Ndipo Samuele anadza kwa Saulo; ndipo Saulo anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinachita lamulo la Yehova.


kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe?


Mukanitu kuti mukadziwitse ndithu, ndi kudziwa ndi kuona mbuto m'mene akhalitsa, ndi amene adamuona m'menemo; chifukwa anandiuza kuti iye achita mochenjera ndithu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa