Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwake, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kuchotsa mutu wanga? Taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi chitseko. Kodi mapazi a mbuye wake samveka dididi pambuyo pake?