Ndipo Yehova anayang'anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamchitira iye monga ananena.
1 Samueli 2:21 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana aamuna atatu, ndi ana aakazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana amuna atatu, ndi ana akazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adadalitsadi Hana, ndipo adabala ana aamuna atatu ndi ana aakazi aŵiri. Ndipo mnyamata uja Samuele ankakula akutumikira Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anamukomera mtima Hana. Anakhala ndi pathupi ndi kubereka ana aamuna atatu ndi ana aakazi awiri. Ndipo Samueli ankakula pamaso pa Yehova. |
Ndipo Yehova anayang'anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamchitira iye monga ananena.
Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.
Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.
Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.
Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.
Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namutcha dzina lake Samisoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa.