Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 13:14 - Buku Lopatulika

Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala chikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pake; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ake, chifukwa inu simunasunge chimene Yehova anakulamulirani.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala chikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pake; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ake, chifukwa inu simunasunga chimene Yehova anakulamulirani.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Chauta wadzifunira yekha munthu wa kumtima kwake. Chauta wamsankha munthuyo kuti akhale mfumu yolamulira anthu ake, chifukwa inu simudatsate zimene Iye adakulamulani.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Yehova wapeza munthu wapamtima pake ndipo wamusankha kukhala mtsogoleri wa anthu ake chifukwa inu simunasunge malamulo a Yehova.”

Onani mutuwo



1 Samueli 13:14
21 Mawu Ofanana  

Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.


Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lake lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israele, chifukwa chake ndidzasewera pamaso pa Yehova.


Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,


Ndipo anasankha Davide mtumiki wake, namtenga kumakola a nkhosa.


pakuti chuma sichili chosatha; kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo.


Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Imvani mau a Yehova wa makamu.


Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.


amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo.


Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.


Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.


Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israele.


Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.


Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.


Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m'dzanja lako.


Ndipo kudzali, pamene Yehova anachitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israele;


Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.